Psalms 133

Salimo la Davide. Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu.

1Onani, nʼkokoma ndi kokondweretsa ndithu
pamene abale akhala pamodzi mwachiyanjano!
2Zili ngati mafuta amtengowapatali othiridwa pa mutu,
otsikira ku ndevu,
ku ndevu za Aaroni,
oyenderera mpaka mʼkhosi mwa mkanjo wake.
3Zili ngati mame a ku Heremoni
otsikira pa Phiri la Ziyoni.
Pakuti pamenepo Yehova amaperekapo dalitso,
ndiwo moyo wamuyaya.
Copyright information for NyaCCL